Kawumitsidwe ka tsabola pogwilitsa tchito dzuwa

Akatenga nthawi yayitali asanawume, tsabola amayamba kumela ndele. Izi zimapangitsa kuti tsabola awonongeke. Powonjezela apa, ndelezi zimapangitsanso kuti tsabola achite chukwu. Chuku chimawopsyeza miyoyo ya anthu. Kuti tsabola wathu awume mwachangu komanso mwaukhondo, titha kugwilitsa ntchito makina omwe amayendela mphamvu yadzuwa. Makinawa ali m’mitundu ndi makulidwe osiyanasiyana. Koma kapangidwe ndi kagwilitsidwe ntchito kake sikamasiyana. Mu kanema uyu, tiphunzila za momwe tingapangile ndi kugwilisila ntchito makina osalila zambiri powumitsa tsabola.

Current language
Chichewa / Nyanja
Need a language?
If you would like this video translated into other languages, please contact kevin@accessagriculture.org
Uploaded
7 years ago
Duration
11:35
Produced by
Agro-Insight