Kumanga khola la kalulu
Uploaded 2 years ago | Loading
11:04
Alimi a dziko la Kenya akutionetsa mmene amamangira khola la akalulu ndi zipangizo zosavuta kupeza. Chifukwa choti akalulu satuluka thukuta kapena kupuma mwachangu akatenthedwa, amavutika padzuwa. Kotero nkofunika kuika khola panthunzi. Khola la mmwamba limateteza akalulu ku makoswe komanso ndowe zimagwera pansi mmalo modzadzana mukhola. Mphembezu zimatha kuvulaza ana akalulu, otchani mphira ndikuwaza mchere kuthamangitsa nyererezi. Ndibwinonso kuononga zulu zonse zanyerere zoyandikira. Mfundo izi ndi zina zambiri zitha kukuthandizani kuweta akalulu, ulimi omwe ukukomdedwa tsopano ndipo utha kukupezetsani phindu lochuluka.
Current language
Chichewa / Nyanja
Produced by
Environmental Alert, DAES, KENFAP, Egerton University