Kudyeta akalulu
Uploaded 4 years ago | Loading
12:40
Anthu ambiri amaweta akalulu chifukwa malo ochepa, nthawi yochepa, kotero amatha kupeza ndalama mwamsanga. Mukhola, kalulu amadya zomwe mwampatsa. Ngati mukufuna kalulu akule bwino ndi kuswana kwambiri, ndi kofunika kumudyetsa bwino.Umitsani zomerazi musanawapatse akalulu tsiku lotsatira.Izi zimathandiza kuti akalulu asatsegule mmimba komwe kumayamba ndi tidzilombo tokhala mmasamba onyowa kapena amame.Powonjezera, kuumitsa kumachotsanso madzi ochepa. Izi zimathandiza kuti akalulu asamatupe mimba.Masamba ena ongothyoledwa kumene amateteza ku matenda. Masamba monga a gwafa ndi nandolo amathetsa kutsegula mmimba. Masamba a Neem ndi Vernonia amathetsa matenda otupa mimba otchedwa coccidiosis.
Current language
Chichewa / Nyanja
Produced by
Songhaï Centre, DEDRAS