Momwe mungapangire malo ozizira otsungira tomato
Uploaded 4 years ago | Loading
5:44
Pamene muthyola tomato mumafuna akhale nthawi yaitali ndiye mwayenera kupeza njira yochepetsera kutentha. Popeza magetsi amakhala ovuta kupezeka kumudzi, njira ziyenera kupezeka zochepetsera kuonongeka kwa tomato. Ndiye tingatani kuti tichepetse kutentha ngati kuli dzuwa? Alimi ena ku Dambatta mdera la Kano ku Nigeria akugwiritsa ntchito zidina pomanga malo ozizira osungiramo tomato.
Current language
Chichewa / Nyanja
Produced by
Countrywise Communication