Kudyetsera mbuzi za mkaka
Uploaded 2 years ago | Loading
9:39
Reference book
Mbuzi zimadya pafupifupi chilichonse. Koma mbuzi zikakhala zomangilira kapena mukhola zimafunika madzi ambiri, kasakaniza wabwino ndi okwanira wachakudya. Mukamazipatsa chakudya tsiku lililonse, mutha kukwaniritsa zakudya zamaguru monga zopatsa mphamvu, zomanga thupi, mavitamini, ndi michere yofunikira. Umitsani udzu kwa masiku atatu musanazidyetse kupewa kutsekula mmimba. Mbuzi za mkaka zimagaya bwino chakudya ndikupeleka mkaka wambiri zikamwa madzi. Zomera zina zimathandiza kupanga mkaka wambiri kusiyana ndi zina., ngati momwe akufotokozera alimi ena a mdziko la Kenya.
Current language
Chichewa / Nyanja
Produced by
Environmental Alert, DAES, KENFAP, Egerton University